Chomwecho mfumu inabwera nifika ku Yordani. Ndipo Ayuda anadza ku Giligala, kuti akakomane ndi mfumu, ndi kumuolotsa mfumu pa Yordani.
1 Samueli 11:15 - Buku Lopatulika Ndipo anthu onse anapita ku Giligala; ndi kumeneko analonga Saulo mfumu pamaso pa Yehova mu Giligala; ndi pamenepo anaphera nsembe zoyamika pamaso pa Yehova; ndi pomwepo Saulo ndi anthu onse a Israele anakondwera kwakukulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anthu onse anapita ku Giligala; ndi kumeneko analonga Saulo mfumu pamaso pa Yehova m'Giligala; ndi pamenepo anaphera nsembe zoyamika pamaso pa Yehova; ndi pomwepo Saulo ndi anthu onse a Israele anakondwera kwakukulu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Aisraele onse adapita ku Giligala ndipo kumeneko adalonga Sauloyo ufumu pamaso pa Chauta. Anthu adapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Chauta, ndipo Saulo pamodzi ndi Aisraele onse adasangalala zedi kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo kumeneko Samueli anakalonga Sauli ufumu pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anthu anapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova, ndipo Sauli ndi Aisraeli onse anachita chikondwerero chachikulu. |
Chomwecho mfumu inabwera nifika ku Yordani. Ndipo Ayuda anadza ku Giligala, kuti akakomane ndi mfumu, ndi kumuolotsa mfumu pa Yordani.
Ndipo anatuma ana a Israele a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, za ng'ombe.
Ndipo Samuele ananena ndi anthu onse, Mumuona kodi iye amene Yehova anamsankha, kuti palibe wina wakufanana naye pakati pa anthu onse? Ndipo anthu onse anafuula, kuti, Akhale ndi moyo mfumuyo.
Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani chimene mudzachita.
Ndipo Samuele anauza Aisraele onse, kuti, Onani ndinamvera mau anu mwa zonse munalankhula ndi ine, ndipo ndinakulongerani mfumu.
Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atumize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti choipa chanu munachichita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, nchachikulu.
Koma anthu anakana kumvera mau a Samuele; nati, Iai, koma tifuna kukhala nayo mfumu yathu;