Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 11:14 - Buku Lopatulika

Ndipo Samuele ananena kwa anthuwo, Tiyeni tipite ku Giligala, kukonzanso ufumu kumeneko.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Samuele ananena kwa anthuwo, Tiyeni tipite ku Giligala, kukonzanso ufumu kumeneko.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono Samuele adauza anthuwo kuti, “Tiyeni tipite ku Giligala, tikatsimikizenso ufumu wa Saulo kumeneko.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo Samueli anati kwa anthuwo, “Tiyeni tipite ku Giligala kuti tikatsimikizenso kuti Sauli ndi mfumu yathu.”

Onani mutuwo



1 Samueli 11:14
8 Mawu Ofanana  

Chomwecho mfumu inabwera nifika ku Yordani. Ndipo Ayuda anadza ku Giligala, kuti akakomane ndi mfumu, ndi kumuolotsa mfumu pa Yordani.


koma musamafuna Betele, kapena kumalowa mu Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.


Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani chimene mudzachita.


Ndipo Samuele anauza Aisraele onse, kuti, Onani ndinamvera mau anu mwa zonse munalankhula ndi ine, ndipo ndinakulongerani mfumu.


Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa taonani Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m'malo mwake.


Ndipo anayenda chozungulira chaka ndi chaka ku Betele, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israele m'malo onse amenewa.