1 Samueli 10:17 - Buku Lopatulika Ndipo Samuele anaitana anthu onse asonkhane kwa Yehova ku Mizipa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Samuele anaitana anthu onse asonkhane kwa Yehova ku Mizipa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Samuele adaitana anthu ku msonkhano wachipembedzo ku Mizipa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Samueli anayitana Aisraeli onse kuti asonkhane pamaso pa Yehova ku Mizipa. |
Pamenepo Yefita anamuka ndi akulu a Giliyadi, ndipo anthu anamuika mkulu wao ndi mtsogoleri wao; ndipo Yefita ananena mau ake onse pamaso pa Yehova ku Mizipa.
Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.
Ndipo anthu onse anapita ku Giligala; ndi kumeneko analonga Saulo mfumu pamaso pa Yehova mu Giligala; ndi pamenepo anaphera nsembe zoyamika pamaso pa Yehova; ndi pomwepo Saulo ndi anthu onse a Israele anakondwera kwakukulu.
Ndipo anayenda chozungulira chaka ndi chaka ku Betele, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israele m'malo onse amenewa.