Awa ndi akulu a nyumba za makolo mwa mibadwo yao, ndiwo akulu anakhala mu Yerusalemu awa.
1 Mbiri 9:3 - Buku Lopatulika Ndipo mu Yerusalemu munakhala a ana a Yuda, ndi a ana a Benjamini, ndi a ana a Efuremu ndi Manase: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'Yerusalemu munakhala a ana a Yuda, ndi a ana a Benjamini, ndi a ana a Efuremu ndi Manase: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ena a ku Yuda, Benjamini, Efuremu ndi Manase amene ankakhala ku Yerusalemu anali motere: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu a ku Yuda, Benjamini ndi Efereimu ndiponso Manase amene anakhala mu Yerusalemu anali awa: |
Awa ndi akulu a nyumba za makolo mwa mibadwo yao, ndiwo akulu anakhala mu Yerusalemu awa.
Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, wa ana a Perezi mwana wa Yuda.
Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ochokera m'mafuko onse a Israele, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israele, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.
Ndipo akulu a anthu anakhala mu Yerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale mu Yerusalemu, mzinda wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m'mizinda ina.