Ndipo Reaya mwana wa Sobala anabala Yahati; ndi Yahati anabala Ahumai, ndi Lahadi. Iwo ndiwo mabanja a Azorati.
1 Mbiri 4:3 - Buku Lopatulika Iwo ndiwo a atate wa Etamu: Yezireele, ndi Isima, ndi Idibasi; ndipo dzina la mlongo wao ndiye Hazeleleponi, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iwo ndiwo a atate wa Etamu: Yezireele, ndi Isima, ndi Idibasi; ndipo dzina la mlongo wao ndiye Hazeleleponi, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Huri naŵa: Etamu amene adabereka Yezireele, Isima ndi Idibasi, ndiponso mlongo wao Hazeleleponi; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana a Etamu anali awa: Yezireeli, Isima ndi Idibasi. Dzina la mlongo wawo linali Hazeleliponi. |
Ndipo Reaya mwana wa Sobala anabala Yahati; ndi Yahati anabala Ahumai, ndi Lahadi. Iwo ndiwo mabanja a Azorati.
ndi Penuwele atate wa Gedori, ndi Ezere atate wa Husa. Awa ndi ana a Huri woyamba wa Efurata atate wa Betelehemu.
Pamenepo anatsikira ku phanga la Etamu amuna zikwi zitatu a ku Yuda, nati kwa Samisoni, Sudziwa kodi kuti Afilisti ndiwo akutilamulira ife? Nchiyani ichi watichitira? Nati iye kwa iwowa, Monga anandichitira ine ndawachitira iwo.