Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.
1 Mbiri 2:3 - Buku Lopatulika Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisuwa Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi Iye anamupha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisuwa Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi Iye anamupha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Yuda naŵa: Eri, Onani, ndi Sela. Ana atatu ameneŵa adamubalira ndi Batisuwa mkazi wa ku Kanani. Tsono Eri mwana wa Yuda anali wa makhalidwe oipa, choncho Chauta adamupha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana a Yuda anali awa: Eri, Onani ndi Sela. Ana atatu awa anabereka ndi mkazi wa Chikanaani, Batisuwa. Eri, mwana woyamba wa Yuda anali woyipa kwambiri pamaso pa Yehova, kotero Yehova anamupha. |
Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.
Ana a Sela mwana wa Yuda: Eri atate wa Leka, ndi Laada atate wa Maresa, ndi mabanja a nyumba ya iwo oomba bafuta wa thonje losansitsa a nyumba ya Asibeya,
Ana aamuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m'dziko la Kanani.
Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.