1 Akorinto 9:9 - Buku Lopatulika Pakuti m'chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamitsa ng'ombe pakupuntha iyo dzinthu. Kodi Mulungu asamalira ng'ombe? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti m'chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamitsa ng'ombe pakupuntha iyo dzinthu. Kodi Mulungu asamalira ng'ombe? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja timaŵerenga m'Malamulowo kuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe pamene ikupuntha tirigu.” Kodi pamene adanena zimenezi, Mulungu adangosamala za ng'ombe zokha? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Popeza analemba mʼMalamulo a Mose kuti, “Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu.” Kodi pamene Mulungu ananena zimenezi ankalabadira za ngʼombe zokha? |
Tirigu wa mkate aperedwa; pakuti samampuntha osaleka; ngakhale kuyendetsapo njinga ya galeta wake, ngakhale kumphwanya ndi ziboda za akavalo ake sapera.
ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?
koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira ntchito iliyonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena ng'ombe yako, kapena bulu wako, kapena zoweta zako zilizonse, kapena mlendo wokhala m'mudzi mwako; kuti wantchito wako wamwamuna ndi wantchito wako wamkazi apumule monga iwe mwini.
Pakuti malembo ati, Usapunamiza ng'ombe yopuntha tirigu. Ndipo Wogwira ntchito ayenera kulipira kwake.