Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Akorinto 9:7 - Buku Lopatulika

Msilikali ndani achita nkhondo, nthawi iliyonse, nadzifunira zake yekha? Aoka mipesa ndani, osadya chipatso chake? Kapena aweta gulu ndani, osadya mkaka wake wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Msilikali ndani achita nkhondo, nthawi iliyonse, nadzifunira zake yekha? Aoka mipesa ndani, osadya chipatso chake? Kapena aweta gulu ndani, osadya mkaka wake wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kodi alipo msilikali womadzipezera yekha zofunika zonse? Kodi alipo munthu wobzala mpesa, koma osadyako zipatso zake? Kodi alipo munthu wokhala ndi ziŵeto, koma osamwako mkaka wake?

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndani angagwire ntchito ya usilikali namadzipezera yekha zofunika zonse? Kodi ndani amadzala mpesa koma wosadyako zipatso zake? Ndani amaweta nkhosa koma wosamwako mkaka wake?

Onani mutuwo



1 Akorinto 9:7
16 Mawu Ofanana  

Wosunga mkuyu adzadya zipatso zake; wosamalira ambuyake adzalemekezedwa.


mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya; ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.


Koma munda wanga wamipesa, uli pamaso panga ndiwo wangatu; nacho chikwicho, Solomoni iwe, koma olima zipatso zake azilandira mazana awiri.


ndipo padzakhala, chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene zidzapatsa, iye adzadya mafuta; pakuti mafuta ndi uchi adzadya yense wosiyidwa pakati padziko.


Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.


Chakudya chao chizifanana, osawerengapo zolowa zake zogulitsa.


Ndipo ndani munthuyo anaoka munda wampesa osalawa zipatso zake? Amuke nabwerere kunyumba yake, kuti angafe kunkhondo, nangalawe munthu wina zipatso zake.


Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino;


Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.


Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro:


Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;