Mutilole tipite ku Yordani, tikatengeko aliyense mtengo, tidzimangire malo komweko, tikhalepo. Nati, Mukani.
1 Akorinto 9:6 - Buku Lopatulika Kapena kodi ife tokha, Barnabasi ndi ine tilibe ulamuliro wakusagwira ntchito? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kapena kodi ife tokha, Barnabasi ndi ine tilibe ulamuliro wakusagwira ntchito? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi ine ndi Barnabasi, ndife tokha oyenera kugwira ntchito zamanja kuti tizidzipezera tokha zotisoŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi kapena ine ndekha ndi Barnaba ndiye tikuyenera kugwira ntchito kuti tipeze zotisowa? |
Mutilole tipite ku Yordani, tikatengeko aliyense mtengo, tidzimangire malo komweko, tikhalepo. Nati, Mukani.
ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'chilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;
Ndipo mbiri yao inamveka m'makutu a Mpingo wakukhala mu Yerusalemu; ndipo anatuma Barnabasi apite kufikira ku Antiokeya;
Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mzindawo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnabasi, ndipo anawapirikitsa iwo m'malire ao.
Ndipo anamutcha Barnabasi, Zeusi; ndi Paulo, Heremesi, chifukwa anali wotsogola kunena.
ndipo popeza anali wa ntchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira ntchito; pakuti ntchito yao inali yakusoka mahema.
Ndipo Yosefe, wotchedwa ndi atumwi Barnabasi (ndilo losandulika mwana wa chisangalalo), Mlevi, fuko lake la ku Kipro,
Koma akaoneka wina ngati wotetana, tilibe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Mpingo wa Mulungu.
Pakuti mukumbukira, abale, chigwiritso chathu ndi chivuto chathu; pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.