Mlongo wanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa; ngati kasupe wotsekedwa, ndi chitsime chopikiza.
1 Akorinto 9:5 - Buku Lopatulika Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi si koyenerera kwa ife kuti ŵaakazi azitsagana nafe pa maulendo athu, monga zikuchitikira ndi atumwi ena ngakhalenso abale a Ambuye ndiponso Kefa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi ife tilibe ulamuliro wotenga mkazi wokhulupirira nʼkumayenda naye monga amachitira atumwi ena ndi abale awo a Ambuye ndiponso Kefa? |
Mlongo wanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa; ngati kasupe wotsekedwa, ndi chitsime chopikiza.
Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? Kodi dzina lake la amake si Maria? Ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda?
Ndipo pofika Yesu kunyumba ya Petro, anaona mpongozi wake ali gone, alikudwala malungo.
Ndipo mpongozi wake wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za iye:
Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.
Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).
Zitapita izi anatsikira ku Kapernao, Iye ndi amake, ndi abale ake, ndi ophunzira ake; nakhala komweko masiku owerengeka.
Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.
Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wamkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkrea;
Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Khristu.
Koma ngati wosakhulupirirayo achoka, achoke. M'milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo. Koma Mulungu watiitana ife mumtendere.
Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.
Koma mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndili ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yake ya iye yekha kwa Mulungu, wina chakuti, wina chakuti.
Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.
Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;
a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.
ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mau.
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.