Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pake adyeko zoyerazo, popeza ndizo chakudya chake.
1 Akorinto 9:4 - Buku Lopatulika Kodi tilibe ulamuliro wa kudya ndi kumwa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi tilibe ulamuliro wa kudya ndi kumwa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi si koyenerera kwa ife kumalandira chakudya ndi chakumwa? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi ife tilibe ulamuliro wakudya ndi kumwa? |
Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pake adyeko zoyerazo, popeza ndizo chakudya chake.
kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.
Ndipo m'nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wantchito ayenera mphotho yake; musachokachoka m'nyumba.
kapena sitinakhale ofuna ulemerero wa kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, tingakhale tinali nayo mphamvu yakukulemetsani monga atumwi a Khristu.
Pakuti mukumbukira, abale, chigwiritso chathu ndi chivuto chathu; pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.