Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani;
1 Akorinto 9:3 - Buku Lopatulika Chodzikanira changa kwa iwo amene andifunsa ine ndi ichi: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chodzikanira changa kwa iwo amene andifunsa ine ndi ichi: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimene ndimaŵayankha ofufuza za ine ndi izi: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kwa iwo wofuna kundizenga milandu ndimawayankha kuti: |
Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani;
Koma ndinawayankha, kuti machitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa chomneneracho.
Ngati wina ayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye.
Ngati sindili mtumwi kwa ena, komatu ndili kwa inu; pakuti chizindikiro cha utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye.
Chifukwa cha ichi ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndili pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa.
popeza mufuna chitsimikizo, cha Khristu wakulankhula mwa ine; amene safooka kwa inu, koma ali wamphamvu mwa inu;
Dziyeseni nokha, ngati muli m'chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha. Kapena simuzindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Mukapanda kukhala osatsimikizidwa.
koma ena alalikira Khristu mochokera m'chotetana, kosati koona, akuyesa kuti adzandibukitsira chisautso m'zomangira zanga.
monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.
Pa chodzikanira changa choyamba panalibe mmodzi anandithangata, koma onse anandisiya; chimenecho chisawerengedwe chowatsutsa.