Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m'chigonjetso.
1 Akorinto 9:25 - Buku Lopatulika Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aliyense wothamanga pa mpikisano wa liŵiro amadziletsa pa zonse. Iwowo amachita zimenezi kuti akalandire mphotho ya nkhata yamaluŵa yotha kufota. Koma mphotho imene ife tidzalandira, ndi yosafota. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense wochita mpikisano amakonzekera mwamphamvu. Amachita izi kuti alandire mphotho yankhata yamaluwa yomwe imafota. Koma ife timachita izi kuti tilandire mphotho yosafota. |
Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m'chigonjetso.
Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.
Koma ngatinso wina ayesana nao m'makani amasewero, samveka korona ngati sanayesane monga adapangana.
komatu wokonda kuchereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;
okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m'chikhulupiriro, m'chikondi, m'chipiriro.
Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.
Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.
kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira mu Mwamba inu,
ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo;
Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.
akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao kumpando wachifumu, ndi kunena,
Ndipo pozinga mpando wachifumu mipando yachifumu makumi awiri mphambu inai, ndipo pa mipandoyo padakhala akulu makumi awiri mphambu anai, atavala zovala zoyera, ndi pamitu pao akorona agolide.