Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Akorinto 8:5 - Buku Lopatulika

Pakuti ngakhalenso iliko yoti yonenedwa milungu, kapena m'mwamba, kapena padziko lapansi, monga iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pakuti ngakhalenso iliko yoti yonenedwa milungu, kapena m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, monga iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ena amati kuli zinthu zina kumwambaku, kapena pansi pano, zimene iwo amazitchula milungu, ndipo anthuwo ali nayodi milungu yambiri, ndi ambuye ambiri.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Popeza kuti ngakhale pali yotchedwa milungu, kaya ndi kumwamba kapena pa dziko lapansi (poti ilipodi milungu yambirimbiri ndi ambuye ambirimbiri),

Onani mutuwo



1 Akorinto 8:5
9 Mawu Ofanana  

Pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa mizinda yako, iwe Yuda; ndi maguwa a nsembe amene mwautsira chamanyazi, alingana ndi kuchuluka kwa miseu ya Yerusalemu, ndiwo maguwa akufukizirapo Baala.


Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula.


Koma ili kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kuvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa mizinda yako, Yuda iwe.


Anamwa vinyo, nalemekeza milungu yagolide, ndi yasiliva, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala.


Chifukwa chake pamene anasonkhana, Pilato ananena kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Barabasi kodi, kapena Yesu, wotchedwa Khristu?


Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m'chibadwidwe chao;


Popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi woopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu.


amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.