Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.
1 Akorinto 8:11 - Buku Lopatulika Pakuti mwa chidziwitso chako wofookayo atayika, ndiye mbale amene Khristu anamfera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mwa chidziwitso chako wofookayo atayika, ndiye mbale amene Khristu anamfera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero amene chikhulupiriro chake nchosalimba kwenikweni, adzatayika chifukwa cha iwe amene uli wodziŵa. Chonsecho tsono iyeyo ndi mbale wako amene Khristu adamufera! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero kuti chifukwa cha chidziwitso chanu mʼbale wofowokayu amene chifukwa cha iye, Khristu anafa, wawonongeka chifukwa cha chidziwitso chanu. |
Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.
Koma ngati iwe wachititsa mbale wako chisoni ndi chakudya, pamenepo ulibe kuyendayendanso ndi chikondano. Usamuononga ndi chakudya chako, iye amene Khristu adamfera.
monga inenso ndikondweretsa onse m'zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha unyunjiwo, kuti apulumutsidwe.
Chifukwa chake, ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama kunthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse mbale wanga.
Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu padziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.