1 Akorinto 7:6 - Buku Lopatulika Koma ichi ndinena monga mwa kulola, si monga mwa kulamulira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ichi ndinena monga mwa kulola, si monga mwa kulamulira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene ndikunena zimenezi, sindikuchita mokulamulani ai, koma mokulolani chabe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikunena zimenezi mokulolani chabe osati mokulamulani. |
Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.
Koma kunena za anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani choyesa iye, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika.
Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndinagiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.
Chimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira.
Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena choonadi cha chikondi chanunso.