Koma Barizilai ananena ndi mfumu, Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kunka ku Yerusalemu?
1 Akorinto 7:29 - Buku Lopatulika Koma ichi nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ichi nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chimene ndikukuuzani, abale, nchakuti nthaŵi yachepa. Kuyambira tsopano anthu okwatira akhale monga ngati sadakwatire. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abale, chimene ndikutanthauza nʼchakuti nthawi yatha. Kuyambira tsopano anthu okwatira akhale ngati sanakwatire. |
Koma Barizilai ananena ndi mfumu, Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kunka ku Yerusalemu?
Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?
Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Yafika nthawi, layandikira tsikulo, wogula asakondwere, ndi wogulitsa asamve chisoni; pakuti mkwiyo ukhalira unyinji wao wonse.
Koma ungakhale ukwatira, sunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwe. Koma otere adzakhala nacho chisautso m'thupi, ndipo ndikulekani.
ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu;
ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.
Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;
Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;
Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.