1 Akorinto 7:26 - Buku Lopatulika Chifukwa chake ndiyesa kuti ichi ndi chokoma chifukwa cha chivuto cha nyengo ino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake ndiyesa kuti ichi ndi chokoma chifukwa cha chivuto cha nyengo yino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chifukwa cha masautso a nthaŵi ino, ndiyesa nkwabwino kuti munthu akhale monga momwe aliri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifukwa cha masautso a masiku ano, ndikuganiza kuti nʼkwabwino kuti munthu akhale monga mmene alili. |
Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi iwo akuyamwitsa ana masiku awo! Pakuti padzakhala chisauko chachikulu padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa.
Koma ungakhale ukwatira, sunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwe. Koma otere adzakhala nacho chisautso m'thupi, ndipo ndikulekani.
Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.
kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika;
Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?