1 Akorinto 7:25 - Buku Lopatulika Koma kunena za anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani choyesa iye, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma kunena za anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani choyesa iye, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kunena za amene sali pa banja, ndilibe lamulo lochokera kwa Ambuye. Koma ndikuuzani maganizo anga, ngati munthu amene Ambuye adandichitira chifundo kuti ndikhale wokhulupirika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano za anamwali: Ine ndilibe lamulo lochokera kwa Ambuye, koma ndipereka maganizo anga monga ngati munthu amene mwachifundo cha Ambuye ndine wodalirika. |
Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.
Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.
Koma ungakhale ukwatira, sunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwe. Koma otere adzakhala nacho chisautso m'thupi, ndipo ndikulekani.
Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.
Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndinagiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.
Chimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira.
Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.