Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu; ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; mwandimasulira zondimanga.
1 Akorinto 7:22 - Buku Lopatulika Pakuti iye amene anaitanidwa mwa Ambuye, pokhala ali kapolo, ali mfulu ya Ambuye: momwemonso woitanidwayo, pokhala ali mfulu, ali kapolo wa Khristu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti iye amene anaitanidwa mwa Ambuye, pokhala ali kapolo, ali mfulu ya Ambuye: momwemonso woitanidwayo, pokhala ali mfulu, ali kapolo wa Khristu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti munthu amene anali kapolo pamene Ambuye adamuitana, ameneyo ndi mfulu ya Ambuye. Momwemonso amene anali mfulu pamene Ambuye adamuitana, ameneyo ndi kapolo wa Khristu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti amene anali kapolo pamene amayitanidwa ndi Ambuye, ndi mfulu wa Ambuye; chimodzimodzinso amene anali mfulu pamene anayitanidwa, ndi kapolo wa Khristu. |
Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu; ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; mwandimasulira zondimanga.
Paulo, kapolo wa Yesu Khristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,
Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, chita nako ndiko.
Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ochuluka.
kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Khristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.
Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Khristu.
Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.
Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.
Akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbika m'mapemphero ake masiku onse chifukwa cha inu, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'chifuniro chonse cha Mulungu.
osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.
monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu.
Simoni Petro, kapolo ndi mtumwi wa Yesu Khristu kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m'chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu:
Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu: