1 Akorinto 7:21 - Buku Lopatulika Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, chita nako ndiko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, chita nako ndiko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi unali kapolo pamene Mulungu adakuitana? Usavutike nazo. Komanso ngati upeza mwai woti ulandire ufulu, uugwiritse ntchito mwaiwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi munali kapolo pamene Mulungu anakuyitanani? Musavutike nazo zimenezi. Koma ngati mutapeza mwayi woti mulandire ufulu, ugwiritseni ntchito mwayiwo. |
Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;
Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.
Pakuti iye amene anaitanidwa mwa Ambuye, pokhala ali kapolo, ali mfulu ya Ambuye: momwemonso woitanidwayo, pokhala ali mfulu, ali kapolo wa Khristu.
Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.
Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.
pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.