1 Akorinto 7:13 - Buku Lopatulika Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupirira, navomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupirira, navomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Momwemonso ngati mkhristu wamkazi ali ndi mwamuna wachikunja, ndipo mwamunayo avomera kukhala naye, mkaziyo asathetse ukwatiwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati mayi wina ali ndi mwamuna wosakhulupirira ndipo mwamunayo walola kukhala pa banja ndi mayiyo, ameneyo asamuleke. |
Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.
Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.