1 Akorinto 6:6 - Buku Lopatulika koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa osakhulupirira? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa osakhulupirira? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Bwanji mkhristu akuimba mlandu mkhristu mnzake, mlanduwo nkuupereka kwa anthu akunja kuti auzenge? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mʼmalo mwake mʼbale atengera ku bwalo la mlandu mʼbale mnzake kukaweruzidwa. Zonsezi pamaso pa akunja! |
Ndipo m'mawa mwake anawaonekera alikulimbana ndeu, ndipo anati awateteze, ayanjanenso, nati, Amuna inu, muli abale; muchitirana choipa bwanji?
Kodi akhoza wina wa inu, pamene ali nao mlandu pa mnzake, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima?
Koma pamenepo pali chosowa konsekonse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mnzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa?
Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?
Ndipo Khristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.