Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.
1 Akorinto 6:12 - Buku Lopatulika Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zinthu zonse nzololedwa kwa ine, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwadi kwa ine, koma sindingalole kuti chilichonse chindigonjetse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mumati, “Ine ndili ndi ufulu wochita chilichonse.” Komatu si zonse zimene nʼzothandiza. “Ndili ndi ufulu wochita chilichonse.” Koma sindidzagonjetsedwa ndi chilichonse. |
Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.
Chifukwa chake Ayuda ananena kwa wochiritsidwayo, Ndi Sabata, ndipo sikuloledwa kwa iwe kuyalula mphasa yako.
Pakuti tidziwa kuti chilamulo chili chauzimu; koma ine ndili wathupi, wogulitsidwa kapolo wa uchimo.
Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu padziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi.
Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachite nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu.
koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.
si chifukwa tilibe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu chitsanzo chanu, kuti mukatitsanze ife.
Iwo ndiwo okhala mawanga pa maphwando anu a chikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu;