Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Akorinto 5:9 - Buku Lopatulika

Ndinalembera inu m'kalata ija, kuti musayanjane ndi achigololo;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndinalembera inu m'kalata uja, kuti musayanjane ndi achigololo;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

M'kalata imene ndidaakulemberani, ndidaakuuzani kuti musamayanjane nawo anthu adama.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndakulemberani mʼkalata yanga kuti musayanjane nawo anthu achigololo.

Onani mutuwo



1 Akorinto 5:9
10 Mawu Ofanana  

Lekani, achibwana inu, nimukhale ndi moyo; nimuyende m'njira ya nzeru.


si konsekonse ndi achigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukatuluke m'dziko lapansi;


Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene anachita ntchito iyi.


Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paska wathu waphedwa, ndiye Khristu;


Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?


Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,


ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse;


Koma ngati wina samvera mau athu m'kalata iyi, yang'anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi.


Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.