Achigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa wootcha mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo.
1 Akorinto 5:6 - Buku Lopatulika Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo palibe choti inu nkunyadira ai. Kodi simuŵadziŵa mau aja akuti, “Chofufumitsira buledi chapang'ono chimafufumitsa mkate wonse?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kudziwa kwanu si kwabwino. Kodi simukudziwa kuti yisiti wochepa amafufumitsa mphumphu yaufa wonse wa tirigu? |
Achigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa wootcha mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo.
Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.
Ufanana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anatenga, nachibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira unatupo wonsewo.
Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?
Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene anachita ntchito iyi.