1 Akorinto 4:6 - Buku Lopatulika Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abale, zimene ndanenazi nzokhudza ine ndi Apolo. Ndifuna kuti zimenezi zikuphunzitseni tanthauzo la mau aja akuti, “Musapitirire zimene Malembo akunena.” Nchifukwa chake musamanyadira wina, ndi kupeputsa mnzake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono abale, ndapereka chitsanzo cha ine mwini ndi Apolo kuti mupindule. Phunzirani kwa ife tanthauzo la mawu akuti, “Musamapitirire zimene Malemba akunena,” kuti musamanyade pamene wina aposa mnzake. |
Siyani munthu, amene mpweya wake uli m'mphuno mwake; chifukwa m'mene awerengedwamo ndi muti?
Ndipo anafika ku Efeso Myuda wina dzina lake Apolo, fuko lake la ku Aleksandriya, munthu wolankhula mwanzeru; ndipo anali wamphamvu m'malembo.
Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza ophunzira ena;
Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.
Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Khristu.
Pakuti kulembedwa, Ndidzaononga nzeru za anzeru, ndi kuchenjera kwa ochenjera ndidzakutha.
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,
Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao;
Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene anachita ntchito iyi.
Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse?
Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tili nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.
Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzivomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru.
osadzitamandira popitirira muyeso mwa machititso a ena; koma tili nacho chiyembekezo kuti pakukula chikhulupiriro chanu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa chilekezero chathu kwa kuchulukira,
Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, ayesere ichinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife.
Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikire, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandire, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simunalandire, mulolana naye bwino lomwe.
Mumayesa tsopano lino kuti tilikuwiringula kwa inu. Tilankhula pamaso pa Mulungu mwa Khristu. Koma zonse, okondedwa, zili za kumangirira kwanu.
Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso;
Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira, sindidzakhala wopanda nzeru; pakuti ndidzanena choonadi; koma ndileka, kuti wina angandiwerengere ine koposa kumene andiona ine, kapena amva za ine.
Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu.
Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake, wosagwiritsa mutuwo,
kuti Uthenga Wabwino wathu sunadze kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu.
Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.