1 Akorinto 4:18 - Buku Lopatulika Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ena mwayamba kudzitukumula, monga ngati sindidzabwerako kwanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ena mwa inu mukudzitukumula, ngati kuti sindingabwere kwanu. |
Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene anachita ntchito iyi.
koma ndipempha kuti pokhala ndili pomwepo, ndisalimbike mtima ndi kulimbika kumene ndiyesa kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tilikuyendayenda monga mwa thupi.
Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso;