1 Akorinto 4:16 - Buku Lopatulika Chifukwa chake ndikupemphani, khalani akutsanza ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake ndikupemphani, khalani akutsanza ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikukupemphani tsono kuti muzinditsanzira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifukwa chake ndikukupemphani kuti munditsanze ine. |
Abale, khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang'anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu.
Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.
Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera;
si chifukwa tilibe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu chitsanzo chanu, kuti mukatitsanze ife.
Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao.