1 Akorinto 4:11 - Buku Lopatulika Kufikira nthawi yomwe ino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kufikira nthawi yomwe yino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mpaka tsopano lino timamva njala ndi ludzu, ndipo ndife ausiŵa. Anthu akutimenya, ndipo tilibe pokhala penipeni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mpaka pano tili ndi njala ndi ludzu, tili ndi sanza, tikuzunzidwa, tilibe nyumba. |
Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.
Ndipo anafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiokeya ndi Ikonio; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulo miyala, namguzira kunja kwa mzinda; namuyesa kuti wafa.
Pamene anawaonetsa mikwingwirima yambiri, anawaika m'ndende, nauza mdindo kuti awasunge bwino.
Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Khristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsa kapena lupanga kodi?
Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.
Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.
mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.