Ndipo iwo adzakhala ndi mantha ndi manyazi, chifukwa cha Kusi, amene anawatama, ndi Ejipito, amene anawanyadira.
1 Akorinto 3:21 - Buku Lopatulika Chifukwa chake palibe mmodzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse nzanu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake palibe mmodzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse nzanu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake pasakhale wina aliyense wonyadira anthu chabe. Zinthu zonse nzanu: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho, wina asanyadire anthu chabe! Zonse ndi zanu, |
Ndipo iwo adzakhala ndi mantha ndi manyazi, chifukwa cha Kusi, amene anawatama, ndi Ejipito, amene anawanyadira.
Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowa nyumba wa dziko lapansi silinapatsidwe kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake mwa lamulo, koma mwa chilungamo cha chikhulupiriro.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?
Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina.
Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu.
Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Yesu Khristu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu.
monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.
Iye wakupambana adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndi iye adzakhala mwana wanga.