Ndipo dziko lapansi linamera udzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wake, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yake, monga mwa mtundu wake; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
1 Akorinto 2:16 - Buku Lopatulika Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize Iye? Koma ife tili nao mtima wa Khristu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize Iye? Koma ife tili nao mtima wa Khristu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndi monga Malembo anenera kuti, “Ndani adadziŵa maganizo a Ambuye, kuti athe kuŵalangiza?” Koma ife tili ndi maganizo a Khristu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti “Ndani anadziwa malingaliro a Ambuye, kuti akhoza kumulangiza Iye.” Koma tili nawo mtima wa Khristu. |
Ndipo dziko lapansi linamera udzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wake, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yake, monga mwa mtundu wake; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
Pakuti ndani waima mu upo wa Yehova, kuti aone namve mau ake? Ndani wazindikira mau anga, nawamva?
Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.
Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzake mau a chidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo: