1 Akorinto 2:11 - Buku Lopatulika Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi za munthu angazidziŵe ndani, osakhala mzimu wa mwiniwake yemweyo umene uli mwa iyeyo? Momwemonso palibe munthu amene angadziŵe za Mulungu, koma Mzimu wa Mulungu Mwini. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi ndani mwa anthu angadziwe maganizo a munthu wina, kupatula mzimu wa munthuyo wokhala mʼkati mwake? Chimodzimodzinso palibe amene adziwa maganizo a Mulungu kupatula Mzimu wa Mulunguyo. |
Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzake mau a chidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo:
Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.