1 Akorinto 16:7 - Buku Lopatulika Pakuti sindifuna kukuonani tsopano popitirira; pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti sindifuna kukuonani tsopano popitirira; pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ulendo umenewo sindifuna kungokuwonani chidule modutsa chabe, koma ndikuyembekeza kukhala nanu kanthaŵi ndithu, Ambuye akalola. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sindikufuna kuti ndikuoneni tsopano mongodutsa chabe, koma ndikuyembekezera kudzakhala nanu kwa kanthawi, ngati Ambuye alola. |
Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.
Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.
koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa.
ndi kupempha masiku onse m'mapemphero anga, ngati nkutheka tsopano mwa chifuniro cha Mulungu, ndione ulendo wabwino, wakudza kwa inu.
Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.
Ndipo m'kulimbika kumene ndinafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhale nacho chisomo chachiwiri;