Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.
1 Akorinto 16:5 - Buku Lopatulika Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Masedoniya; pakuti ndidzapyola Masedoniya; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Masedoniya; pakuti ndidzapyola Masedoniya; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzafika kwanuko nditadutsa dziko la Masedoniya, pakuti ndingodzerako ku Masedoniyako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzafika kwanuko nditadutsa ku Makedoniya pakuti ndikuyembekezera kudzera ku Makedoniyako. |
Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.
Pakuti kunakondweretsa a ku Masedoniya ndi Akaya kuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.
Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.