1 Akorinto 15:8 - Buku Lopatulika ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Potsiriza, pambuyo pa onse adandiwonekeranso ineyo, ngakhale ndili ngati mpolo chabe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Potsiriza pa onse anaonekeranso kwa ine, monga mwana wobadwa nthawi isanakwane. |
Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe chifuniro chake, nuone Wolungamayo, numve mau otuluka m'kamwa mwake.
ndipo ndinamuona Iye, nanena nane, Fulumira, tuluka msanga mu Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine.
Ndipo kunali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kunandiwalira pondizungulira ine kuunika kwakukulu kochokera kumwamba.
Komatu uka, imirira pa mapazi ako; pakuti chifukwa cha ichi ndinaonekera kwa iwe, kukuika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya izi wandionamo Ine, ndiponso ya izi ndidzakuonekeramo iwe;
Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani panjira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.
Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi sindinaone Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye?