Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.
1 Akorinto 15:6 - Buku Lopatulika pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake adaonekera abale opitirira mazana asanu pa nthaŵi imodzi. Ambiri mwa iwowo akalipo, ena adamwalira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pambuyo pake, Iye anaonekera kwa anthu oposa 500 mwa abale pa nthawi imodzi, ndipo ambiri mwa iwo akanali ndi moyo ngakhale kuti ena anagona tulo. |
Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.
Koma mukani, uzani ophunzira ake, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu.
Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;
Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau aakulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo.
Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.
Pakuti ichi tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo.
ndi kunena, Lili kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.