nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu woonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa.
1 Akorinto 15:53 - Buku Lopatulika Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi chaimfa ichi kuvala chosafa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi chaimfa ichi kuvala chosafa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti thupi lotha kuwolali liyenera kusanduka losatha kuwola, ndipo thupi lotha kufali liyenera kusanduka losatha kufa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti chovunda chiyenera kuvala chosavunda, ndi thupi ili lakufa liyenera kuvala losafa. |
nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu woonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa.
kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;
nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.
Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.