Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu; koma Afarisi avomereza ponse pawiri.
1 Akorinto 15:13 - Buku Lopatulika Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Khristunso sanaukitsidwe; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Khristunso sanaukitsidwa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristunso sadauke. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati kulibe kuuka kwa akufa, ndiye kuti ngakhale Khristu sanaukenso. |
Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu; koma Afarisi avomereza ponse pawiri.
Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.
Ndipo si chotero chokha, koma ife tomwe, tili nazo zipatso zoyamba za Mzimu, inde ifenso tibuula m'kati mwathu, ndi kulindirira umwana wathu, ndiwo chiomboledwe cha thupi lathu.
Koma ngati Khristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa?
ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe.
Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu.
chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ake.
Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,
Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;
ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.