Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.
1 Akorinto 15:12 - Buku Lopatulika Koma ngati Khristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngati Khristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono popeza kuti chimene timalalika ndi chakuti Khristu adauka kwa akufa, bwanji ena mwa inu akunena kuti, “Anthu akufa sadzaukanso?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati timalalikira kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa, zikutheka bwanji kuti ena mwa inu azinena kuti kulibe kuuka kwa akufa? |
Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.
Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu; koma Afarisi avomereza ponse pawiri.
ndiwo amene adasokera kunena za choonadi, ponena kuti kuuka kwa akufa kwachitika kale, napasula chikhulupiriro cha ena.