Ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunavine; tinabuma maliro, ndipo inu simunalire.
1 Akorinto 14:7 - Buku Lopatulika Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati chitoliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, chidzazindikirika bwanji chimene chiombedwa kapena kuimbidwa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati chitoliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, chidzazindikirika bwanji chimene chiombedwa kapena kuimbidwa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndi ngati zipangizo zopanda moyo zimene zili ndi liwu, monga toliro kapena zeze. Woziliza akapanda kusiyanitsa bwino maliwu ake, womvera sangadziŵe nyimbo imene ikuimbidwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale mu zinthu zopanda moyo monga chitoliro kapena gitala, zimene zimatulutsa liwu; kodi munthu akhoza kudziwa bwanji nyimbo imene ikuyimbidwa ngati mawu sakumveka mogwirizana bwino? |
Ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunavine; tinabuma maliro, ndipo inu simunalire.
Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzake, ndi kunena, Ife tinakulizirani chitoliro, ndipo inu simunavine ai; tinabuma maliro, ndimo simunalire ai.
Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.
Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikakupindulitsani chiyani, ngati sindilankhula ndi inu kapena m'vumbulutso, kapena m'chidziwitso, kapena m'chinenero, kapena m'chiphunzitso?
Ndipo m'tsogolo mwake mudzafika kuphiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumzindako mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi chisakasa, ndi lingaka, ndi chitoliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera;