Ndipo akunja anatichitira zokoma zosachitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, chifukwa cha mvula inalinkugwa, ndi chifukwa cha chisanu.
1 Akorinto 14:11 - Buku Lopatulika Chifukwa chake, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwa ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwa ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ngati ine sindidziŵa tanthauzo la mau a m'chilankhulo, ndidzakhala mlendo kwa amene akulankhula, ndipo iyenso adzakhala mlendo kwa ine. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono ngati sindingatolepo tanthauzo la zimene wina akuyankhula, ndiye kuti ndine mlendo kwa oyankhulayo ndipo iyeyo ndi mlendo kwa ine. |
Ndipo akunja anatichitira zokoma zosachitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, chifukwa cha mvula inalinkugwa, ndi chifukwa cha chisanu.
Koma pamene akunjawo anaona chilombocho chili lende padzanja lake, ananena wina ndi mnzake, Zoona munthuyu ndiye wambanda. Angakhale anapulumuka m'nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo.
Ilipo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau padziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau.
Kwalembedwa m'chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.
pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse.