Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.
1 Akorinto 13:6 - Buku Lopatulika sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. |
Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.
Ndipo Yetero anakondwera chifukwa cha zabwino zonse Yehova adazichitira Israele, ndi kuwalanditsa m'dzanja la Aejipito.
Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.
Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.
Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!
Usandiseka, mdani wangawe; pakugwa ine ndidzaukanso; pokhala ine mumdima Yehova adzakhala kuunika kwanga.
Ndimo akaipeza, indedi ndinena kwa inu, akondwera nayo koposa ndi makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai zosasokera.
amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.
Potero nchiyani? Chokhacho kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m'choonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m'menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera.
nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera,
Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu;
kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirire choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama.
Ndakondwera kwakukulu kuti ndapeza ena a ana anu alikuyenda m'choonadi, monga tinalandira lamulo lochokera kwa Atate.