Ndipo Yakobo anatcha dzina la malo amenewo, Penuwele: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga.
1 Akorinto 13:12 - Buku Lopatulika Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsopano timaona zinthu ngati m'galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthaŵiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera, koma pa nthaŵiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziŵira ine kotheratu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti tsopano tiona zinthu mosaoneka bwino ngati mʼgalasi loonera; kenaka tidzaziona maso ndi maso. Tsopano ndidziwa mosakwanira koma kenaka ndidzadziwa mokwanira, monga mmene Mulungu akundidziwira ine. |
Ndipo Yakobo anatcha dzina la malo amenewo, Penuwele: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga.
Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa; chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo.
Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, moonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.
monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.
Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.
Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.
Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.
Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene anandigwirira Khristu Yesu.
Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m'kalirole;
Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.