Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira chaulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi mu Yerusalemu, ndi pamaso pa akuluakulu ake.
1 Akorinto 13:10 - Buku Lopatulika Koma pamene changwiro chafika, tsono chamderamdera chidzakhala chabe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pamene changwiro chafika, tsono chamderamdera chidzakhala chabe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa koma changwiro chikadzaoneka, chopereŵeracho chidzatha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma changwiro chikadzaoneka ndipo chopereweracho chidzatha. |
Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira chaulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi mu Yerusalemu, ndi pamaso pa akuluakulu ake.
Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.
Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.
Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene anandigwirira Khristu Yesu.