Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Akorinto 12:7 - Buku Lopatulika

Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsono Mzimu amapereka mphatso kwa aliyense kuti ipindulire onse.

Onani mutuwo



1 Akorinto 12:7
11 Mawu Ofanana  

Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire Ine ntchito ya nsembe.


Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu.


Momwemo inunso, popeza muli ofunitsitsa mphatso za Mzimu, funani kuti mukachuluke kukumangirira kwa Mpingo.


Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwe.


koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi zidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime.


Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira.