1 Akorinto 12:23 - Buku Lopatulika ndipo zimene tiziyesa zochepa ulemu m'thupi, pa izi tiika ulemu wochuluka woposa; ndi zinthu zosakoma zikhala nacho chokometsera choposa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo zimene tiziyesa zochepa ulemu m'thupi, pa izi tiika ulemu wochuluka woposa; ndi zinthu zosakoma zikhala nacho chokometsera choposa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ziwalo zimene timaziyesa zotsika, ndizo timazilemekeza kopambana. Ndipo ziwalo za thupi lathu zimene zili zochititsa manyazi, ndizo timaziveka kopambana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo ziwalo zathupi zimene timaziyesa zopanda ulemu, ndizo timazilemekeza kwambiri. Ndipo ziwalo zosaoneka bwino ndizo zimalandira ulemu wapadera. |
Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amaliseche: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira matewera.
Koma zokoma zathu zilibe kusowa; koma Mulungu analumikizitsa thupi, napatsa ulemu wochuluka kwa chosowacho;
koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso.
Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali;