Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Akorinto 12:2 - Buku Lopatulika

Mudziwa kuti pamene munali amitundu, munatengedwa kunka kwa mafano aja osalankhula, monga munatsogozedwa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mudziwa kuti pamene munali amitundu, munatengedwa kunka kwa mafano aja osalankhula, monga munatsogozedwa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mukudziŵa kuti pamene munali akunja, anthu ankakusokezani mwa njira izi ndi izi, kukukokerani ku mafano osalankhula.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Inu mukudziwa kuti pamene munali akunja, ankakusocheretsani mʼnjira zosiyanasiyana ndi kukukokerani ku mafano osayankhula.

Onani mutuwo



1 Akorinto 12:2
15 Mawu Ofanana  

Pakamwa ali napo, koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya;


manja ali nao, koma osagwira; mapazi ali nao, koma osayenda; kapena sanena pammero pao.


Pakamwa ali napo koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya;


Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwake, nukhala chilili; pamalo pakepo sudzasunthika; inde, wina adzaufuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zovuta zake.


Mafanowa akunga mtengo wakanjedza, wosemasema, koma osalankhula; ayenera awanyamule, pakuti sangathe kuyenda. Musawaope; pakuti sangathe kuchita choipa, mulibenso mwa iwo kuchita chabwino.


Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.


Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.


Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m'chibadwidwe chao;


Pakuti iwo okha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu anali otani; ndi kuti munatembenukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weniweni wamoyo,


Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.


podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu:


Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;