Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawirikawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu ena.
1 Akorinto 12:1 - Buku Lopatulika Koma za mphatso zauzimu, abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma za mphatso zauzimu, abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abale, ndifuna kuti muzindikire bwino za mphatso za Mzimu Woyera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano abale anga okondedwa, sindikufuna mukhale osadziwa za mphatso za Mzimu. |
Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawirikawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu ena.
Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;
Ngati wina ayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye.
Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za chisautso chathu tinakomana nacho mu Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;
Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;
Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.
Koma ichi chimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.