Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Akorinto 11:6 - Buku Lopatulika

Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ngati mkazi sazivala kanthu kumutu, kunali bwino atangodula tsitsi lake. Koma popeza kuti nchamanyazi kwa mkazi kumeta mpala, kapena kudula tsitsi lake, ndiyetu azivala kanthu kumutu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ngati mkazi saphimba kumutu kwake, ndiye kuti amete tsitsi lake. Ngati nʼchamanyazi kwa mkazi kungoyepula kapena kumeta mpala, ndiye kuti aphimbe kumutu kwake.

Onani mutuwo



1 Akorinto 11:6
5 Mawu Ofanana  

Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m'manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.


Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m'ngalawa ku Siriya, pamodzi naye Prisila ndi Akwila; popeza anameta mutu wake mu Kenkrea; pakuti adawinda.


Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wovula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa.


Pakuti mwamuna sayenera kuvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.


Mkazi asavale chovala cha mwamuna, kapena mwamuna asavale chovala cha mkazi; pakuti aliyense wakuchita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye.